# asf/2016520.xml.gz
# nya/2016520.xml.gz


(src)="1"> 7 Seek the Kingdom , Not Things
(trg)="2"> 7 Muzifuna - funa Ufumu , Osati Zinthu Zakuthupi

(src)="2"> Jesus taught us to ‘ seek first the Kingdom , ’ not material things .
(trg)="3"> Yesu anatiphunzitsa kuti ‘ tizifuna - funa Ufumu coyamba ’ osati zinthu zakuthupi .

(src)="3"> How can we avoid the snare of materialism and simplify our life so that we can pursue more important spiritual interests ?
(trg)="4"> Kodi tingapewe bwanji msampha wokonda zinthu zakuthupi ?
(trg)="5"> Nanga tingacepetse bwanji zocita zathu mu umoyo kuti tiike zinthu zauzimu patsogolo ?

(src)="4"> Consider Jesus ’ encouraging words in the portion of his Sermon on the Mount found at Matthew 6 : 25 - 34 .
(trg)="6"> M’nkhani ino , tikambilana mau olimbikitsa a Yesu amene anakamba pa Ulaliki wake wa pa Phili wolembedwa pa Mateyu 6 : 25 - 34 .

(src)="5"> 13 Why Must We “ Keep on the Watch ” ?
(trg)="7"> 13 N’cifukwa Ciani Tiyenela ‘ Kukhalabe Maso ’ ?

(src)="6"> As Christians , we must take seriously Jesus ’ admonition to “ keep on the watch ” in these last days .
(trg)="8"> Popeza ndife Akhiristu , sitifunika kupepusa malangizo a Yesu akuti ‘ tikhalebe maso ’ m’masiku ano otsiliza .

(src)="7"> To do that , we need to guard against negative influences that could cause us not to be alert and vigilant with respect to Jesus ’ coming .
(trg)="9"> ( Mat .
(trg)="10"> 24 : 42 ) Kuti ticite zimenezi , tiyenela kupewa zinthu zimene zingatilepheletse kukhala maso kuti tisazindikile kubwela kwa Yesu .

(src)="8"> This article explains how we can avoid being distracted from our watchfulness .
(trg)="11"> Nkhaniyi ifotokoza mmene tingapewele zinthu zimene zingatilepheletse kukhala maso .

(src)="9"> 21 Grateful Recipients of God’s Undeserved Kindness
(trg)="14"> 21 Tiziyamikila Kukoma Mtima Kwakukulu Kumene Tinalandila

(src)="10"> 26 Spread the Good News of Undeserved Kindness
(trg)="15"> 26 Lalikilani Uthenga Wabwino Wokamba za Kukoma Mtima

(src)="11"> These two articles examine many of the ways that we benefit from Jehovah’s undeserved kindness .
(trg)="16"> Nkhani ziŵilizi zifotokoza mmene timapindulila ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova .

(src)="12"> They also explain why our deep gratitude for these expressions of love should move us to make known to others how they too can benefit from Jehovah’s undeserved kindness .
(trg)="17"> Zifotokozanso cifukwa cake kuyamikila cikondi cimene Mulungu wationetsa m’njila zosiyana - siyana , kuyenela kutilimbikitsa kuuzako ena mmene angapindulile ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova .
(trg)="18"> 31 Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

# asf/2016522.xml.gz
# nya/2016522.xml.gz


(src)="1"> “ We all received . . . undeserved kindness upon undeserved kindness . ” ​ — JOHN 1 : 16 .
(trg)="2"> 1 : 16 .

(src)="2"> SONGS : 95 , 13
(trg)="3"> NYIMBO : 95 , 13

(src)="3"> What is the greatest expression of Jehovah’s undeserved kindness toward mankind ?
(trg)="4"> Kodi njila yaikulu koposa imene Yehova waonetsela kukoma mtima kwakukulu kwa anthu ni iti ?

(src)="4"> How can we show that we are no longer ruled by sin but by undeserved kindness ?
(trg)="5"> Tingaonetse bwanji kuti tsopano tikulamulidwa ndi kukoma mtima kwakukulu osati ucimo ?

(src)="5"> What blessings come to us as a result of Jehovah’s undeserved kindness ?
(trg)="6"> Ni madalitso a bwanji amene timapeza cifukwa ca kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova ?

(src)="6"> 1 , 2 . ( a ) Describe Jesus ’ illustration of the owner of the vineyard . ( b ) How does the story illustrate the qualities of generosity and undeserved kindness ?
(trg)="7"> 1 , 2 . ( a ) Fotokozani fanizo la Yesu la mwini munda wa mpesa . ( b ) Kodi fanizoli liwonenetsa bwanji khalidwe la kuwolowa manja ndi kukoma mtima kwakukulu ?

(src)="7"> A WINEGROWER went to the marketplace early one morning to hire men to work in his vineyard .
(trg)="8"> TSIKU lina , munthu wina amene anali ndi munda wa mpesa anacelela ku msika kukasakila anthu aganyu .

(src)="8"> The men he found agreed to the wage he offered and went to work .
(trg)="9"> Anawauza malipilo amene adzawapatsa ndipo anthuwo anavomela .

(src)="9"> The owner needed more workers , however , and returned to the marketplace throughout the day to hire more and more men , offering a fair wage even to those whom he hired at the end of the afternoon .
(trg)="10"> Koma popeza kuti mwini munda wa mpesayo anali kufuna anchito ambili , anapitanso ku msika maulendo angapo kukasakila anchito ena .

(src)="10"> When evening came , he gathered the workers together to give them their wages , and he gave the same amount to each of them , whether they had labored many hours or just one .
(trg)="11"> Iye analonjeza kuti anchito onse adzawapatsa malipilo oyenelela , ngakhale amene anagwila nchito kwa ola limodzi .
(trg)="12"> Madzulo , mwini munda wa mpesa uja anaitanitsa anchitowo kuti awapatse malipilo .

(src)="11"> When those first hired realized this , they complained .
(trg)="13"> Iye anali woolowa manja ndipo anapeleka malipilo ofanana kwa anchito onse , kaya anaseŵenza tsiku lonse kapena ola limodzi cabe .

(src)="12"> The winegrower replied : ‘ Did you not agree to the wage I offered ?
(trg)="15"> Mwini munda wa mpesayo anawafunsa kuti : ‘ Nakupatsani malipilo amene tinapangana , si conco ?

(src)="13"> Do I not have the right to give all my workers whatever I want ?
(trg)="16"> Kodi n’kosaloleka kupatsa anchito anga onse malipilo amene nifuna ?

(src)="14"> Are you envious because I am generous ? ’ ​ — Matt . 20 : 1 - 15 , ftn .
(trg)="17"> Kapena mwacita nsanje cifukwa cakuti ndine woolowa manja ? ’ — Mat .
(trg)="18"> 20 : 1 - 15 .

(src)="15"> Jesus ’ parable reminds us of one of Jehovah’s qualities that is often mentioned in the Bible ​ — his “ undeserved kindness . ”
(trg)="19"> Fanizo la Yesu limatikumbutsa khalidwe la Yehova lochulidwa kambili m’Baibulo .
(trg)="20"> Khalidwe limeneli ni “ kukoma mtima kwakukulu . ”

(src)="16"> ( Read 2 Corinthians 6 : 1 . )
(trg)="21"> ( Ŵelengani 2 Akorinto 6 : 1 . )

(src)="17"> The workers who had labored only one hour did not seem to merit receiving the full wage , but the owner of the vineyard showed them extraordinary kindness .
(trg)="22"> Ena angaganize kuti anchito amene anaseŵenza ola limodzi anafunika kulandila ndalama yocepa kuposa enawo .
(trg)="23"> Koma mwini mundayo anaonetsa khalidwe la kukoma mtima kwakukulu kwa anchito amene anaseŵenza nthawi yocepa .

(src)="18"> Regarding the word for “ undeserved kindness , ” which is translated “ grace ” in many Bible versions , one scholar wrote : “ The whole basic idea of the word is that of a free and undeserved gift , of something given to a man unearned and unmerited . ”
(trg)="24"> Pokamba za liwu limene linamasulidwa kuti “ kukoma mtima kwakukulu , ” katswili wina anakamba kuti : “ Mau amenewa makamaka amakamba za mphatso yaulele imene yapatsidwa kwa munthu amene sanaiseŵenzele , ndiponso amene si woyenelela kuilandila . ”

(src)="19"> 3 , 4 .
(trg)="25"> 3 , 4 .

(src)="20"> Why and how has Jehovah shown undeserved kindness toward all mankind ?
(trg)="26"> N’cifukwa ciani Yehova anaonetsa anthu onse kukoma mtima kwakukulu ?
(trg)="27"> Nanga anacita bwanji zimenezo ?

(src)="21"> The Scriptures speak of “ the free gift of God’s undeserved kindness . ”
(trg)="28"> Baibulo imakamba za “ mphatso yaulele ya kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu . ”
(trg)="29"> ( Aef .

(src)="22"> Why and how does Jehovah bestow this “ free gift ” ?
(trg)="30"> 3 : 7 ) Kodi Yehova anapeleka bwanji “ mphatso yaulele ” imeneyi ?
(trg)="31"> Nanga n’cifukwa ciani ?

(src)="23"> If we met all of Jehovah’s requirements perfectly , his kindness toward us would be deserved .
(trg)="32"> Sembe kuti timacita zonse zimene Yehova amafuna popanda kulakwitsa ciliconse , kukoma mtima kwake kukanatiyenelela .

(src)="24"> As it is , we fail to do so .
(trg)="33"> Koma timalephela kucita zimenezo .

(src)="25"> Thus , wise King Solomon wrote : “ There is no righteous man on earth who always does good and never sins . ”
(trg)="34"> Ndiye cifukwa cake , Mfumu yanzelu Solomo inati : “ Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amacita zabwino zokhazokha osacimwa . ”

(src)="26"> The apostle Paul likewise stated : “ All have sinned and fall short of the glory of God , ” and “ the wages sin pays is death . ”
(trg)="35"> ( Mlal .
(trg)="36"> 7 : 20 ) Mtumwi Paulo nayenso anakamba kuti : “ Onse ndi ocimwa ndipo ndi opeleŵela pa ulemelelo wa Mulungu . ”

(src)="27"> That is what we deserve .
(trg)="37"> Anakambanso kuti “ malipilo a ucimo ndi imfa . ”

(src)="28"> Jehovah , however , expressed his love toward fallen mankind in an incomparable act of undeserved kindness .
(trg)="39"> Popeza kuti Yehova amakonda anthu kwambili , anatumiza “ Mwana wake wobadwa yekha ” kuti adzatifele .

(src)="29"> He sent his greatest gift of all , “ his only - begotten Son , ” to earth to die in our behalf .
(trg)="41"> ( Yoh .
(trg)="42"> 3 : 16 ) Paulo anakamba kuti Yesu ‘ anamuveka ulemelelo ndi ulemu ngati cisoti cacifumu cifukwa cakuti anazunzika mpaka imfa .

(src)="30"> So Paul wrote concerning Jesus that he is “ now crowned with glory and honor for having suffered death , so that by God’s undeserved kindness he might taste death for everyone . ”
(trg)="43"> Zimenezi zinamucitikila kuti mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu , alaŵe imfa m’malo mwa munthu aliyense . ’
(trg)="44"> ( Aheb .

(src)="31"> Yes , “ the gift God gives is everlasting life by Christ Jesus our Lord . ” ​ — Rom . 6 : 23b .
(trg)="45"> 2 : 9 ) Zoona , “ mphatso imene Mulungu amapeleka ndi moyo wosatha kudzela mwa Khristu Yesu Ambuye wathu . ” — Aroma 6 : 23b .

(src)="32"> 5 , 6 .
(trg)="46"> 5 , 6 .

(src)="33"> What are the results when we are ruled ( a ) by sin ?
(trg)="47"> N’ciani cimacitika ngati tilamulidwa ndi ( a ) ucimo ?

(src)="34"> ( b ) by undeserved kindness ?
(trg)="48"> ( b ) kukoma mtima kwakukulu ?

(src)="35"> How did humans inherit the sinful , dying condition that plagues us all ?
(trg)="49"> N’cifukwa ciani ndife ocimwa ndipo timafa ?

(src)="36"> The Bible explains : “ By the trespass of the one man [ Adam ] death ruled as king ” over Adam’s descendants .
(trg)="50"> Baibulo imati : “ Cifukwa ca ucimo wa munthu mmodziyo [ Adamu ] imfa inalamulila monga mfumu ” kwa mbadwa za Adamu .

(src)="37"> Happily , though , we can choose no longer to be ruled , or dominated , by sin .
(trg)="51"> ( Aroma 5 : 12 , 14 , 17 ) Komabe , cokondweletsa n’cakuti tili ndi ufulu wokana kulamulidwa ndi ucimo .

(src)="38"> By exercising faith in Christ’s ransom sacrifice , we place ourselves under the rule of Jehovah’s undeserved kindness .
(trg)="52"> Tikakhulupilila nsembe ya dipo la Khiristu , ndiye kuti tasankha kuti tizilamulidwa ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova .

(src)="39"> How so ?
(trg)="53"> Kodi zimenezi zimatheka bwanji ?

(src)="40"> “ Where sin abounded , undeserved kindness abounded still more .
(trg)="54"> Baibulo imati : “ Pamene ucimo unawonjezeka , kukoma mtima kwakukulu kunasefukilanso .

(src)="41"> To what end ?
(trg)="55"> Cifukwa ciani ?

(src)="42"> So that just as sin ruled as king with death , so also undeserved kindness might rule as king through righteousness leading to everlasting life through Jesus Christ . ” ​ — Rom .
(trg)="56"> Kuti mmene ucimo unalamulila monga mfumu pamodzi ndi imfa , momwemonso kukoma mtima kwakukulu kulamulile monga mfumu kudzela m’cilungamo .

(src)="43"> 5 : 20 , 21 .
(trg)="57"> Zimenezi zicitike kuti moyo wosatha ubwele kudzela mwa Yesu Khristu Ambuye wathu . ” — Aroma 5 : 20 , 21 .

(src)="44"> Even though we remain sinners , we need not resign ourselves to having sin dominate our lives .
(trg)="58"> Ngakhale kuti ndife ocimwa , sitiyenela kulola ucimo kutilamulila .

(src)="45"> When we do give in to sin , we will ask Jehovah for his forgiveness .
(trg)="59"> Cotelo , ngati tacita chimo , tiyenela kupempha Yehova kuti atikhululukile .

(src)="46"> Paul warned Christians : “ Sin must not be master over you , seeing that you are not under law but under undeserved kindness . ”
(trg)="60"> Paulo anaticenjeza kuti : “ Ucimo usakhale mbuye kwa inu , cifukwa simuli pansi pa cilamulo koma pansi pa kukoma mtima kwakukulu . ”

(src)="47"> Therefore , we come under the rule of undeserved kindness .
(trg)="61"> ( Aroma 6 : 14 ) Conco , tili pansi pa ulamulilo wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu .

(src)="48"> With what result ?
(trg)="62"> Kodi zimenezi zimatipindulitsa bwanji ?

(src)="49"> Paul explained : “ The undeserved kindness of God . . . trains us to reject ungodliness and worldly desires and to live with soundness of mind and righteousness and godly devotion amid this present system of things . ” ​ — Titus 2 : 11 , 12 .
(trg)="63"> Paulo anakamba kuti : ‘ Kukoma mtima kwakukulu [ kwa Mulungu ] . . . kwatiphunzitsa kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko , koma kukhala amaganizo abwino , acilungamo ndi odzipeleka kwa Mulungu m’nthawi ino . ’ — Tito 2 : 11 , 12 .

(src)="50"> 7 , 8 .
(trg)="64"> 7 , 8 .

(src)="51"> What does it mean that Jehovah’s undeserved kindness is “ expressed in various ways ” ?
(trg)="65"> Kodi Malemba atanthauza ciani pamene akamba kuti Yehova wasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu “ m’njila zosiyanasiyana ? ”

(src)="52"> ( See opening pictures . )
(trg)="66"> ( Onani zithunzi kuciyambi kwa nkhani ino . )

(src)="53"> The apostle Peter wrote : “ To the extent that each one has received a gift , use it in ministering to one another as fine stewards of God’s undeserved kindness that is expressed in various ways . ”
(trg)="67"> Mtumwi Petulo analemba kuti : “ Molingana ndi mphatso imene aliyense walandila , igwilitseni nchito potumikilana monga oyang’anila abwino amene alandila kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu , kumene wakusonyeza m’njila zosiyanasiyana . ”
(trg)="68"> ( 1 Pet .

(src)="54"> What does that mean ?
(trg)="69"> 4 : 10 ) Kodi lembali litanthauza ciani ?

(src)="55"> That whatever the nature of the trials we may face in life , Jehovah can enable us to cope with them .
(trg)="70"> Litanthauza kuti pa mavuto alionse amene tingakumane nao , Yehova adzatipatsa mphamvu zofunikila kuti tikwanitse kupilila .
(trg)="71"> ( 1 Pet .

(src)="56"> There will always be an expression of God’s kindness that will match each trial .
(trg)="72"> 1 : 6 ) Iye adzatipatsa ciliconse cofunikila n’colinga cakuti tisagonje tikakumana ndi ciyeso .

(src)="57"> Indeed , Jehovah’s undeserved kindness is expressed in various ways .
(trg)="73"> Kukamba zoona , Yehova wationetsa kukoma mtima kwake kwakukulu m’njila zosiyana - siyana .

(src)="58"> The apostle John wrote : “ We all received from his fullness , even undeserved kindness upon undeserved kindness . ”
(trg)="74"> Mtumwi Yohane analemba kuti : “ Tonsefe tinalandila zinthu kucokela pa zoculuka zimene ali nazo .
(trg)="75"> Tinalandila kukoma mtima kwakukulu kosefukila . ”
(trg)="76"> ( Yoh .

(src)="59"> The various expressions of Jehovah’s kindness result in our receiving many blessings .
(trg)="77"> 1 : 16 ) Popeza kuti Yehova amaonetsa kukoma mtima kwake kwakukulu m’njila zosiyana - siyana , timalandila madalitso ambili .

(src)="60"> What are some of them ?
(trg)="78"> Kodi ena mwa madalitso amenewa ni ati ?

(src)="61"> How do we benefit from Jehovah’s undeserved kindness , and how can we show our gratitude for it ?
(trg)="79"> Timapindula bwanji ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova ?
(trg)="80"> Nanga tingaonetse bwanji kuti timayamikila ?

(src)="62"> Being forgiven of our sins .
(trg)="81"> Mulungu amatikhululukila macimo .

(src)="63"> Because of Jehovah’s undeserved kindness , we have our sins forgiven , provided we repent and continue to put up a hard fight against our sinful inclinations .
(trg)="82"> Cifukwa ca kukoma mtima kwake kwakukulu , Yehova amatikhululukila macimo .
(trg)="83"> Koma amacita zimenezo ngati ndife olapa , ndipo tikuyesetsa kulimbana ndi zilakolako zoipa .

(src)="64"> ( Read 1 John 1 : 8 , 9 . )
(trg)="84"> ( Ŵelengani 1 Yohane 1 : 8 , 9 . )

(src)="65"> God’s mercy should fill us with gratitude and move us to glorify him .
(trg)="85"> Tiyenela kuyamikila Mulungu ndi kum’tamanda cifukwa ca cifundo cake .

(src)="66"> Writing to fellow anointed Christians , Paul stated : “ [ Jehovah ] rescued us from the authority of the darkness and transferred us into the kingdom of his beloved Son , by means of whom we have our release by ransom , the forgiveness of our sins . ”
(trg)="86"> Paulo analembela Akhiristu anzake odzozedwa kuti : “ [ Yehova ] anatilanditsa ku ulamulilo wa mdima , n’kutisamutsila mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa .
(trg)="87"> Mwa Mwana wakeyo , tinamasulidwa ndi dipo , kutanthauza kuti macimo athu anakhululukidwa . ”
(trg)="88"> ( Akol .

(src)="67"> Being forgiven of our sins opens the door to many other wonderful blessings .
(trg)="89"> 1 : 13 , 14 ) Popeza kuti Mulungu amatikhululukila macimo , tilinso na mwayi wolandila madalitso ena ambili - mbili .

(src)="68"> What do we enjoy because of God’s undeserved kindness ?
(trg)="90"> Ni mwayi wabwanji umene tili nawo cifukwa ca kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu ?

(src)="69"> Having a peaceful relationship with God .
(trg)="91"> Timakhala pa unansi wabwino na Mulungu .

(src)="70"> In our sinful state , from birth we were enemies of God .
(trg)="92"> Ife anthu timabadwa tili kale pa udani ndi Mulungu .

(src)="71"> Paul acknowledged this : “ When we were enemies we became reconciled to God through the death of his Son . ”
(trg)="93"> Komabe , Paulo anati : “ Pamene tinali adani , tinayanjanitsidwa kwa Mulungu kudzela mu imfa ya Mwana wake . ”

(src)="72"> This reconciliation enables us to be at peace with Jehovah .
(trg)="94"> ( Aroma 5 : 10 ) Kuyanjanitsidwa kumeneko kunatithandiza kuti tikhale pamtendele ndi Yehova .

(src)="73"> Paul links this privilege to Jehovah’s undeserved kindness , stating : “ Now that we [ Christ’s anointed brothers ] have been declared righteous as a result of faith , let us enjoy peace with God through our Lord Jesus Christ , through whom we also have obtained access by faith into this undeserved kindness in which we now stand . ”
(trg)="95"> Paulo anagwilizanitsa mwayi umenewu ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova pamene anauza odzozedwa anzake kuti : “ Cotelo , popeza tsopano tayesedwa olungama cifukwa cokhala ndi cikhulupililo , tiyeni tikhale pa mtendele ndi Mulungu kudzela mwa Ambuye wathu Yesu Khristu .
(trg)="96"> Mwa ameneyunso , ndiponso cifukwa ca cikhulupililo , takhala ndi ufulu woloŵa m’kukoma mtima kwakukulu , mmene tilimo tsopano . ”

(src)="74"> What a blessing this is !
(trg)="97"> ( Aroma 5 : 1 , 2 ) Umenewu ni mwayi wa mtengo wapatali .

(src)="75"> Expressions of God’s undeserved kindness : The privilege of hearing the good news ( See paragraph 11 )
(trg)="98"> Mmene Mulungu waonetsela kukoma mtima kwake kwakukulu : Mwayi womvela uthenga wabwino ( Onani ndime 11 )

(src)="76"> How do the anointed bring the “ other sheep ” to righteousness ?
(trg)="99"> Kodi odzozedwa amathandiza bwanji a “ nkhosa zina ” kukhala olungama ?

(src)="77"> Being brought to righteousness .
(trg)="100"> Timaonedwa olungama pamaso pa Mulungu .

(src)="78"> All of us are unrighteous by nature .
(trg)="101"> Ife tonse timabadwa osalungama .

(src)="79"> But the prophet Daniel foretold that during the time of the end , “ those having insight , ” the anointed remnant , would be “ bringing the many to righteousness . ”
(trg)="102"> Mneneli Danieli analemba kuti m’nthawi ya mapeto , “ anthu ozindikila , ” kapena kuti odzozedwa , ‘ adzathandiza anthu ambili kukhala olungama . ’

(src)="80"> ( Read Daniel 12 : 3 . )
(trg)="103"> ( Ŵelengani Danieli 12 : 3 . )