# am/101989285.xml.gz
# ny/101989285.xml.gz


(src)="1"> ከኤድስ የከፋ ነገር
(trg)="1"> Chinachake Choipitsitsa Kuposa Aids

(src)="2"> “ ምርመራው በሽታው እንዳለብህ አረጋግጧል ።
(trg)="2"> “ Kufufuza kunali kovomereza .

(src)="3"> ኤድስ ይዞሃል ። ”
(trg)="3"> Inu muli ndi AIDS . ”

(src)="5"> ይህ የሆነው ባለፈው ዓመት አንድ ቀን ነበር ።
(trg)="4"> Mawu amenewo a dokotala wanga anamveka m’mutu mwanga pamene ndinanyamula lamya tsiku lina chaka chatha .

(src)="6"> የአምላክን ምክር ሰምቼ ተግባራዊ አድርጌው ቢሆን ኖሮ ይህ ባልደረሰብኝ ነበር !
(trg)="5"> Ngati kokha ndinamvetsera ku uphungu wa Mulungu ndi kuwugwiritsira ntchito , ndikanapeŵa zimenezi !

(src)="7"> በዋሽንግተን ክፍለ ሀገር ውስጥ የይሖዋ ምስክር ሆኜ ነበር ያደግሁት ።
(trg)="6"> NDINALEEDWA monga mmodzi wa Mboni za Yehova mu boma la Washington , ndipo makolo anga anatsimikizira kuti ndinadziŵa zimene zinali zifuno za Mulungu .

(src)="8"> ወላጆቼ አምላክ የሚፈልግብንን ነገሮች በሚገባ አሳውቀውኝ ነበር ።
(trg)="7"> Chotero chinadza monga chodabwitsa kwa anthu ambiri pamene ndinayamba kukhala mosiyana ndi kuphunzitsidwa kwanga kwa uchichepere .

(src)="10"> በትምህርት ቤት ውስጥ ባሉ ልጆች መወደድ በጣም የምመኘው ነገር ሆነ ።
(trg)="8"> Kukondedwa ndi achichepere ena a pa sukulu kunali chovuta kwa ine .

(src)="11"> በነሱ ዘንድ ተቀባይነት ለማግኘት ያላደረግሁት ጥረት አልነበረም ።
(trg)="9"> Ndinayesera mitundu yonse ya zinthu kukhala wolandirika .

(src)="12"> ሙከራዬ ሁሉ ሳይሳካልኝ ስለቀረ 15 ዓመት ሲሆነኝ ሁሉም ነገር ተስፋ አስቆራጭ ሆኖ ታየኝ ።
(trg)="10"> Inde , palibe chirichonse chomwe chinagwira ntchito , ndipo podzafika nthaŵi imene ndinali wazaka 15 , ndinazindikira kuti chirichonse chinali chopanda chiyembekezo .

(src)="13"> እንዲያውም ራሴን ልገድል ሞክሬ ነበር ፤ ግን ሳይሳካልኝ ቀረ ።
(trg)="11"> Ndinakhoza ngakhale kuyesera , kudzipha , mosaphula kanthu .

(src)="14"> ሁኔታውን የሚያሻሽልልኝ መስሎኝ ትንባሆና ማሪዋና ማጨስ ጀመርኩ ።
(trg)="12"> Ndikumaganiza kuti zinthu zingakhaleko bwino , ndinayamba kugwiritsira ntchito fodya ndi mbanje .

(src)="15"> ግን አላሻሻለልኝም ።
(trg)="13"> Ayi ndithu , sizinatero .

(src)="16"> ከጥቂት ጊዜ በኋላ የይሖዋን ድርጅት ለመተውና ደስታ የሚገኝበት ሌላ ቦታ ለመፈለግ ወሰንኩ ።
(trg)="14"> Pambuyo pa kanthaŵi , ndinagamulapo kuchoka m’gulu la Yehova ndi kuyang’ana kwinakwake kaamba ka chimwemwe .

(src)="17"> ለትምህርት ቤት ጓደኞቼ ከእንግዲህ ወዲያ የይሖዋ ምስክር አይደለሁም ብዬ ነገርኳቸው ።
(trg)="15"> Ndinalengeza kwa mabwenzi anga a kusukulu kuti sindinalinso mmodzi wa Mboni za Yehova , ndipo anawonekera kuchikonda icho .

(src)="20"> ውሎ አድሮ ሥራ አገኘሁ ።
(trg)="16"> Moyo wa Chisembwere , Wosakhazikika

(src)="21"> እንዲሁም በርካሽ ዋጋ ኪራይ በሚገኝበት ሰካራሞችና ሴተኛ አዳሪዎች በሚኖሩበት ሰፈር ውስጥ አንድ አፓርታማ ተከራየሁ ።
(trg)="17"> Potsirizira pake ndinapeza ntchito ndiponso nyumba yokhala m’mzera cha kunsi , kumene akazi a ganyu onse ndi achigololo ankachezera .

(src)="22"> እነሱም አጭበርብሮ ገንዘብ ማግኘት እንዴት ቀላል እንደሆነ ይነግሩኝ ጀመር ።
(trg)="18"> Iwo anapitiriza kundiwuza ine mmene chinaliri chopepuka kuchita machenjera kaamba ka ndalama .

(src)="23"> በነሱ እርዳታ ብዙም ሳልቆይ እኔም ዘዴውን ለመድኩት ።
(trg)="19"> Ndi thandizo lawo , sichinatenge nthaŵi yotalikira ndisanaphunzire kumwerekerako .

(src)="24"> በሁሉም ሰው መወደድና መደሰት የምፈልግ ሰው ነበርኩ ፤ አሁን ግን የማንም መጠቀሚያ የሆንኩና በጣም የተከፋሁ ሰው ሆንኩ ።
(trg)="20"> Ndinasintha kuchoka pa munthu yemwe anafuna kukondedwa ndi aliyense ndi kukhala wachimwemwe kukhala winawake yemwe ankagwiritsiridwa ntchito ndi aliyense ndipo ndinali wopanda chimwemwe kwenikweni .

(src)="26"> ወላጆቼና የበፊቱ ኑሮዬ ናፈቁኝ ።
(trg)="21"> Ndinafuna kusintha , kubwerera kumudzi ndi kuyambanso .

(src)="27"> ስለዚህ ይሖዋ እንዲረዳኝ ጸለይኩ ።
(trg)="22"> Ndinakhumba makolo anga ndi moyo womwe ndinali nawo poyambapo .

(src)="28"> የከበደኝ ነገር ወደ ወላጆቼ ሄጄ ይቅርታ እንዲያደርጉልኝ መጠየቁ ነበር ።
(trg)="23"> Chotero ndinapemphera kwa Yehova kaamba ka thandizo .

(src)="29"> ምስጋና ይግባቸውና ልባቸው ይቅርታ ለማድረግ ፈቃደኛ ሆነ ።
(trg)="24"> Mbali yovuta inali kufikira makolo anga ndi kupempha chikhululukiro chawo .

(src)="30"> ክርስቲያን ሽማግሌዎች አነጋገሩኝና ወደ ጉባኤ ለመመለስ ያለኝን ምኞት ገለጽኩላቸው ።
(trg)="25"> Moyamikirika , iwo anachipeza kukhala chabwino kundikhululukira .

(src)="31"> ይህ ለነሱም ሆነ ለኔ ቀላል አልነበረም ።
(trg)="26"> Akulu Achikristu anakumana nane , ndipo ndinalongosola chikhumbo changa kaamba ka kubwezeretsedwa mu mpingo .

(src)="32"> ዕፅ መውሰዴ ካመጣብኝ ችግር ሌላ ከባድ የአባለዘር በሽታም ነበረብኝ ።
(trg)="27"> Sichinali chopepuka kwa iwo kapena kwa ine .

(src)="33"> የመረመረኝ ሐኪም ወደ ሐኪም ቤት ሳልሄድ አንድ ወር ብቻ እንኳን ቆይቼ ቢሆን ኖሮ እሞት እንደነበረ ነገረኝ ።
(trg)="28"> Osati kokha kuti ndinali ndi mavuto ndi ziyambukiro za pambali za kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa koma ndinali nditatenganso matenda oipitsitsa opatsirana mwa kugonana .

(src)="34"> በራሴ ላይ ምን ዓይነት ጣጣ ነው ያመጣሁት !
(trg)="29"> Dokotala wanga anandiwuza ine kuti ngati ndinayembekeza kwa mwezi umodzi wokha , ndikafa .

(src)="35"> ከጊዜ በኋላ ከውገዳ ተመለስኩ ።
(trg)="30"> Ndi zoipa zotani nanga zimene ndinadziikamo inemwini !

(src)="36"> እንዲያውም ከጎረቤት ጉባኤ አንዲት ወጣት አገባሁ ።
(trg)="31"> M’kupita kwa nthaŵi , ndinabwezeretsedwa , ndipo ndinakhoza ngakhale kukwatira mkazi wachichepere kuchokera mu mpingo wapafupi .

(src)="37"> ነገሮች እየተሻሻሉ ሄዱ ።
(trg)="32"> Zinthu zinkasintha .

(src)="38"> እኔ ግን አሁንም ቢሆን የይሖዋን ፍቅር አላደነቅሁትም ።
(trg)="33"> Komabe , sindinayamikirebe chikondi cha Yehova .

(src)="39"> ብርታት ለማግኘት በይሖዋ ላይ በመመካት ፈንታ ነገሮችን እኔው ራሴ ለመሥራት እሞክር ነበር ።
(trg)="34"> Ndinkayesera kuchita zinthu m’njira yanga m’malo mwa kudalira pa iye kaamba ka mphamvu .

(src)="40"> ሁለት ዓመት ከማይሞላ ጊዜ በኋላ በጾታ ብልግና ምክንያት ከሚስቴ ጋር ተፋታሁ ፤ እንዲሁም ተወገድኩ ።
(trg)="35"> Zochepera pa zaka ziŵiri pambuyo pake , ndinasudzula mkazi wanga ndi kuchotsedwanso kaamba ka chisembwere .

(src)="41"> ከአንዳንድ ዓለማውያን ጋር መዋል ጀምሬ ነበር ።
(trg)="36"> Ndinali nditagwirizana ndi anthu a kudziko .

(src)="42"> በመጀመሪያ ላይ ምንም ጉዳት የማያስከትል ይመስል ነበር ፤ ይሁን እንጂ “ ክፉ ባልንጀርነት መልካሙን አመል ያጠፋል ” የሚለው የማይለወጠው ቅዱስ ጽሑፋዊ ማስጠንቀቂያ ትክክል ሆኖ ተገኘ ። ​ — 1 ቆሮንቶስ 15 : 33
(trg)="37"> Chinali kokha chabwinopo pa nthaŵi yoyamba , koma chenjezo la m’Malemba limatsimikizira kukhala lolondola : “ Mayanjano oipa aipsya makhalidwe okoma . ” — 1 Akorinto 15 : 33 .

(src)="43"> እንደገና ወደ መጥፎ ድርጊት መዘፈቅ
(trg)="38"> Kumira Mwakuya M’kuipa Kachiŵirinso

(src)="44"> ካለሁበት ርቄ ከሄድኩ ቤተሰቤን ያን ያህል አልጎዳም ብዬ አሰብኩ ።
(trg)="39"> Mwa kusamukira kutali , ndinalingalira kuti sindikakhoza kuvulaza banja langa mochulukira .

(src)="45"> በሳን ፍራንሲስኮ ካሊፎርኒያ ውስጥ ሥራና መኖሪያ ለማግኘት ምንም አልተቸገርኩም ።
(trg)="40"> Ndinalibe vuto la kupeza ntchito ndi malo okhalako mu San Francisco , California .

(src)="46"> አንድ የአደንዛዥ ዕፅ ነጋዴ ዕፅ በማከፋፈል ሥራ እንድቀጠር ጠየቀኝ ።
(trg)="41"> Wogulitsa mankhwala ogodomalitsa anandiloŵetsa ntchito yoperekera mankhwala ogodomalitsa .

(src)="47"> የመጡትን ‘ አዲስ የአደንዛዥ ዕፅ ዓይነቶች ’ ሁሉ በመውሰድ በነፃ ከሚሞክርለት የተመረጠ ቡድን መሐል ነበርኩ ።
(trg)="42"> Ndinalinso pakati pa gulu lake lotchuka lomwe linkayesera , kwaulere , ‘ mankhwala ogodomalitsa okonzedwa ’ chatsopano onse omwe ankadza .

(src)="48"> አሁን ደግሞ በሌላ መንገድ ታዋቂ ሆንኩ ።
(trg)="43"> Tsopano ndinali ndi kutchuka kwa mtundu wina watsopano .

(src)="49"> የሚያውቁኝ ሁሉ ( ብዙ የሚያውቁኝ ሰዎች ነበሩ ) ዕፅ እንዳለኝ ያውቃሉ ።
(trg)="44"> Aliyense yemwe anandidziŵa ( ndipo panali ochepera ) anadziŵa kuti ndinali ndi mankhwala ogodomalitsa .

(src)="50"> በመንገድ ላይ ፣ ቡና ቤት ውስጥ ፣ ሥራ ቦታም ሳይቀር አንድ ነገር ለመግዛት ወደኔ ይመጡ ነበር ።
(trg)="45"> Iwo ankakhoza kudza kwa ine mu makwalala , m’malo omwera moŵa , ndipo ngakhale pa ntchito , akumafuna kugula chinachake kuchokera kwa ine .

(src)="51"> ከዚህም ሌላ በጾታ ብልግና ውስጥ ለመዘፈቅ ጊዜ አልፈጀብኝም ፤ ይህ እንደተወደድኩ እንዲሰማኝ የሚያደርገኝ መንገድ ነበረ ።
(trg)="46"> Pambali pa icho , sindinachedwe m’pangono pomwe kudziloŵetsa m’chisembwere ; inali njira kaamba ka ine ya kudzimva wokondeka .

(src)="52"> ከፍተኛ ተወዳጅነትም ነበረኝ ።
(trg)="47"> Ndipo ndinakondedwa kwambiri .

(src)="53"> በጾታ ግንኙነት በመጠቀም ሌሎች ሰዎች የምፈልገውን እንዲያደርጉልኝ የሚያስችለኝን ብልሃት ተማርኩ ።
(trg)="48"> Ndinaphunzira kugwiritsira ntchito anthu ena kupyolera m’kugonana kuti ndipeze zinthu zomwe ndinafuna .

(src)="54"> ለብዙ ዓመታት በዚህ ዓይነት ኖርኩ ።
(trg)="49"> Kwa zaka zingapo ndinakhala mwanjirayi .

(src)="56"> የሚመረምረኝ ሐኪም በሽታዬ ምን እንደሆነ አላወቀም ።
(trg)="50"> Ndimakumbukira bwino lomwe pa chochitika chimodzi ndikumadwala malungo okulira ndi kukhala wofooka kwambiri .

(src)="57"> ከጊዜ በኋላ ትኩሳቱ ለቀቀኝ ።
(trg)="51"> Dokotala wanga sanadziŵe chomwe ndinadwala .

(src)="58"> እስከ ሦስት ዓመት ድረስ ምን እንደያዘኝ ላውቅ አልቻልኩም ነበር ።
(trg)="52"> M’kupita kwa nthaŵi anatha .

(src)="59"> በዚህ ጊዜ ውስጥ አጋንንትም ያስቸግሩኝ ጀመር ።
(trg)="53"> Sindinakhoze kudziŵa chomwe ndinawunikiridwako kufikira zaka zitatu pambuyo pake .

(src)="60"> እንዲያውም አንድ ጊዜ ጥቃት አድርሰውብኝ ነበር ።
(trg)="54"> Mkati mwa nthaŵiyi , ndinayambanso kukhala ndi vuto ndi ziwanda , pa nthaŵi imodzi ndinawukiridwa m’chenicheni .

(src)="61"> ጋኔኑ ሰውነቴ ውስጥ ሊገባብኝ እየሞከረ እንዳለ ተሰማኝ ።
(trg)="55"> Ndinadzimva kuti chiwanda chinkayesera kuloŵa m’thupi langa .

(src)="62"> አንድም ቃል ለመተንፈስ እንዳልችል ይታገለኛል ።
(trg)="56"> Kunali kumenyera kukakamiza liwu lirilonse kumveka kutuluka mkamwa mwanga .

(src)="63"> ሞክሬ ሞክሬ በመጨረሻ “ ይሖዋ እርዳኝ ! ”
(trg)="57"> Ndinayesera ndi kuyesera kufikira potsirizira pake ndinali wokhoza kufuula , “ Ndithandizeni Yehova ! ”

(src)="64"> ብዬ ለመጮህ ቻልኩ ።
(trg)="58"> Chiwandacho mwamsanga chinachoka .

(src)="66"> ምን እንደተሰማኝ ገምቱ !
(trg)="59"> Tangolingalirani mmene ndinadzimverera !

(src)="67"> በጾታ ብልግና የተጨማለቀ ኑሮ እየኖርኩና ለራሴ ብቻ እያሰብኩ እያለሁ ይሖዋ እንዲረዳኝ ለመጣራት ግን ደፈርኩ !
(trg)="60"> Pano ndinali kukhala ndi moyo wachisembwere chakuya ndi kuganizira kokha za inemwini , komabe ndinali ndi lingaliro la kuitanira pa Yehova kaamba ka thandizo !

(src)="68"> በጣም አሳፈረኝ ።
(trg)="61"> Ndinadzimva wamanyazi kwenikweni .

(src)="69"> ይሖዋ ይረዳኛል ብዬ እንዴት ልገምት እችላለሁ ?
(trg)="62"> Nchifukwa ninji ndinalingalira kuti Yehova akakhoza kundithandiza ?

(src)="70"> ከፍተኛ የመንፈስ ጭንቀት ውስጥ ገባሁ ።
(trg)="63"> Ndinaloŵa m’kupsyinjika kwakuya .

(src)="71"> አንድ ሰው እንዲገድለኝ በመፈለግ ሆነ ብዬ ሕይወቴን አደጋ ላይ እጥል ጀመር ።
(trg)="64"> Ndinaika moyo wanga m’ngozi modzifunira , ndikumafuna winawake kuti andiphe .

(src)="72"> የመለወጥ ፍላጎት
(trg)="65"> Chikhumbo cha Kusintha

(src)="73"> አንድ ቀን ከጓደኞቼ ጋር ግብዣ ላይ እያለን ስለ ዓለም ጉዳዮች መወያየት ጀመርን ።
(trg)="66"> Tsiku lina , pamene tinkayenda ndi mabwenzi ena , tinadziloŵetsa m’kukambitsirana ponena za zochitika zadziko .

(src)="74"> ስለ ወደፊቱ ሁኔታ ምን ታስባለህ ?
(src)="75"> ብለው ሲጠይቁኝ ሳላውቀው አምላክ ለምድርና ለሕዝቦቹ ያለውን ዓላማ ነገርኳቸው ።
(trg)="67"> Pamene iwo anandifunsa ine chomwe ndinalingalira ponena za mtsogolo , ndinadzipeza inemwini ndikuwawuza ponena za chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi ndi anthu ake .

(src)="76"> በጣም ተገረሙ ።
(trg)="68"> Iwo anazizwa .

(src)="77"> አንደኛው ግን በጣም ተናደደና ግብዝ ነህ አለኝ ።
(trg)="69"> Koma munthu mmodzi anakwiya nane kwenikweni ndi kunditcha wonyenga !

(src)="78"> ፍጹም ትክክል ነበር ።
(trg)="70"> Iye anali wolondola kotheratu .

(src)="79"> ሁለት ዓይነት ኑሮ ነበር የምኖረው ።
(trg)="71"> Ndinali kukhala moyo wapaŵiri .

(src)="80"> በልቤ ግን ብቸኛው አዳኛችን ይሖዋ መሆኑንና ድርጅቱም ሊኖርበት የሚገባ ብቸኛ ቦታ መሆኑን አውቅ ነበር ።
(trg)="72"> Komabe , mozama mkati mwa mtima wanga , ndinadziŵa kuti Yehova anali chipulumutso chathu chokha ndi kuti gulu lake linali malo okha okhalako .

(src)="81"> በዚህ ጊዜ ገደማ የኔና ከኔ ጋር የነበሩት የሌሎቹ ሕይወት መለወጥ ጀመረ ።
(trg)="73"> Chifupifupi pa nthaŵiyi moyo wanga ndi miyoyo ya ondizungulira inayamba kusintha .

(src)="82"> ብዙዎቹ ጓደኞቼ ኤድስ ይዟቸው አልጋ መያዝ ጀመሩ ።
(trg)="74"> Ambiri a mabwenzi anga ankabwera ndi AIDS .

(src)="83"> በአንድ ወቅት ጤነኛ የነበሩ ሰዎች ቀስ በቀስ መንምነው ሲሞቱ ማየት ይከብድ ነበር ።
(trg)="75"> Chinali chovuta kuwona anthu omwe pa nthaŵi imodzi anali aumoyo akumawonda pang’onopang’ono ndi kufa .

(src)="84"> እነሱን ማጽናናት አቃተኝ ።
(trg)="76"> Ndinadzimva wopanda thandizo kuwatonthoza iwo .

(src)="85"> የተሻለ የሕይወት መንገድ እንዳለ ማወቄ ደግሞ ይበልጥ የሚያበሳጭ ነበር ።
(trg)="77"> Chinali makamaka chokhumudwitsa chifukwa chakuti ndinadziŵa njira yabwino ya moyo .

(src)="86"> በዚያን ጊዜ ወደ ይሖዋ ፍቅር መመለስ እንደምፈልግ አወቅሁ ።
(trg)="78"> Ndinadziŵa kenaka kuti ndinafuna kubwerera ku chikondi cha Yehova .

(src)="87"> ግን እንዴት ?
(trg)="79"> Koma motani ?

(src)="88"> ይሖዋ እንዲረዳኝ መጸለይ ጀመርኩ ።
(trg)="80"> Ndinayamba kupemphera kwa Yehova kaamba ka thandizo .

(src)="89"> መጸለይ ይከብደኝ ነበር ።
(trg)="81"> Chinali chovuta kwenikweni kuchichita .

(src)="90"> ያሳፍረኛል ፤ ቆሻሻ እንደሆንኩም ይሰማኛል ።
(trg)="82"> Ndinadzimva wamanyazi kwenikweni ndi wodetsedwa .

(src)="91"> አንድ ቀን ስልክ ተደወለልኝ ።
(trg)="83"> Tsiku lina ndinalandira lamya .

(src)="92"> አክስቴ ነበረች ፤ ካየኋት ከዘጠኝ ዓመታት በላይ አልፏል ።
(trg)="84"> Inachokera kwa azakhali anga , omwe sindinawonepo pa zaka zoposa zisanu ndi zinayi .

(src)="93"> መጥታ ልትጠይቀኝ እንደምትፈልግ ነገረችኝ ።
(trg)="85"> Iwo anafuna kubwera kudzandiwona ine .

(src)="94"> ምንም እንኳን የወላጆቼ ዓይነት ሃይማኖት ባይኖራትም ሕይወቴን ለመለወጥና እንደገና የይሖዋ ምስክር ለመሆን የምፈልግ መሆኑን ነገርኳት ።
(trg)="86"> Ngakhale kuti iwo sanagawane chikhulupiriro cha makolo anga , ndinawauza iwo kuti ndinafuna kusintha moyo wanga ndi kubwerera kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova .

(src)="95"> ከልቤ መሆኑን ስለተረዳች ልትረዳኝ ፈለገች ።
(trg)="87"> Iwo anakhoza kuwona kutsimikizira kwanga ndipo anafuna kuthandiza .

(src)="96"> ለመመለስ የፈጀብኝ ረጅም ጊዜ
(trg)="88"> Njira Yaitali Yobwerera

(src)="97"> አክስቴ መንፈሴ እስኪረጋጋ ድረስ ከእርሷ ጋር እንድኖር ጋበዘችኝ ።
(trg)="89"> Azakhali anga anandiitana ine kusamukira kwawo kufikira nditabwereranso m’njira yanga yabwino .

(src)="98"> ይህ ሊረዳኝ ይችል እንደሆነ ስትጠይቀኝ እዚያው ቆሜ አለቀስኩ ።
(trg)="90"> Pamene anandifunsa kaya ngati chimenecho chikathandiza , ndinangoima pamenepo ndi kulira .

(src)="99"> ያስፈልገኝ የነበረው የመውጫ መንገድ ይህ እንደሆነ አውቅ ነበር ።
(trg)="91"> Ndinadziŵa kuti iyi inali njira yotulukira yomwe ndinafunikira , chotero ndinasiya oyanjana nawo anga akale .

(src)="101"> ቀጣዮቹ ጥቂት ወራት ቀላል አልነበሩም ፤ ቢሆንም ይሖዋ እንድቋቋማቸው እንደሚረዳኝ እተማመን ነበር ።
(trg)="92"> Miyezi yotsatira yoŵerengeka siinali yopepuka , koma ndinali ndi chidaliro kuti Yehova akakhoza kundithandiza ine kuzipyola izo .